Pamene kwangotsala miyezi yowerengeka kuti dziko lino lichititse chisankho cha pulezidenti mabungwe omwe siaboma pansi pa mgwirizano wawo olimbikitsa nkhani za demokalase ndi ulamuliro wabwino mdziko muno lachinayi achita ziwonetsero mumzinda wa Blantyre zosonyeza kukwiya ndi boma la pulezidenti Joyce Banda.
Wapampando wa wamgwirizanowo a Voice Mhone ati mwa zina anakonza ziwonetserozi pofuna kudziwa momwe boma linayendetsera ndalama zomwe linapeza litagulitsa ndege, komwe kunapita chimanga cha boma chomwe ndi chokwana 30,000 metric tonnes komanso kuti boma lichitepo kanthu msanga pazotsatira zakubedwa kwa ndalama za boma. Anthu ochepa okha ndi omwe anali nawo pa ziwonetserozo zomwe zinayambira ku Kanjedza mpaka ku ma ofesi abwanamkubwa wa mzindawu a Ted Nandolo komwe anakapereka chikalata cha madandaulowa. Malinga ndi a Mhone ziwonetserozi ndi chiyambi cha zochitika zosiyanasiyana zomwe mgwirizanowu wakonza kuti zichitike m'madera osiyanasiyana mdziko muno powonetsa kusakondwa ndi boma.
Pakadali pano m'modzi mwa anthu omwe amatsatira momwe zinthu zikuyendera mdziko muno a Henry Kachaje ati ziwonetsero sizingathandize kuthetsa mavuto mdziko muno. A Kachaje ati nkofunika kuti nyumba yamalamulo ikhaledi yoyima payokha.