Bungwe lowona za chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lati litsekulanso malo ena olembetsera kalembera wa zisankho ku malo omwe anthu sanathe kulembetsa kwa masiku 14 kamba ka mavuto ena.
M'chikalata chomwe bungweli latulutsa chati pakadali pano bungweli lidziperekanso mpata kuti anthu apitirize kulembetsa kumapeto kwa masiku omwe akonzedwa pakakhala zovuta zina. Malinga ndi bungweli, Izi zidzichitika pakatha masiku khumi ndi anayi omwe anakhazikitsidwa. Bungwe la MEC lachenjezanso anthu omwe adalembetsa kale kuti asapititenso kukalembetsa ponena kuti ndi mlandu omwe munthu amayenera kulipira ndalama zokwana 5 hundred thousand kapena kukakhala ku ndende zaka ziwiri.