Amayi a mpingo wa katolika mu parishi ya Chisitu mu arkidayosizi ya Blantyre ati miyoyo yawo ya chikhristu ikuzama pomwe akumakhala ndi mwambo wa nsembe ya ukaristia mwezi ndi mwezi.
Mkhalapampando wa bungweli mu parishiyi mayi Brandina Mbendera anena izi loweruka pambuyo pa mwambo wa nsembe ya ukaristia ya bungweli.
Iwo ati kupatula kuzamitsa moyo wawo wa chikhristu amayiwa amalimbikitsananso mu njira zosiyanasiyana.
Polankhula mowalimbikitsa amayiwa, mlangizi wa bungwe la amayi mparishiyi SisterMeria Chabweraanati amayi akuyenera kukhala a chikhulupiliro cholimba ndipo asabwelere m’mbuyo pamene akumana ndi zokhumudwitsa.