Anthu khumi afa ndipo ena asanu ndi awiri apulumutsidwa boti lomwe anakwera litagubuduzika pa Nyanja ya Indian mdziko la Sri Lanka.
Anthu omwe anali mu botili ati anakachita nawo chikondwelero cha zipembedzo chomwe chimachitikira mtawuni ya Beruwala kummwera kwa likulu la dzikolo ndipo ngoziyi yachitika pomwe amachokera ku malowa.
Malipoti News 24ati chiwerengero cha anthu omwe anali mu botilo sichikudziwika koma padakali pano kafukufuku adakali mkati wofufuza ngati pali ena omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.