Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Ntchembere Zandonda Zawononga Kwambiri Mbewu mu Machinga ADD

$
0
0

Ofesi yoyang’anira ntchito za ulimi m’maboma a m’chigawo cha ku m’mawa cha dziko lino ya MachingaADDyadandaula kaamba ka zilombo zina zomwe zikuwoneka ngati ntchembere zandonda zomwe ati zakhudza mbewu za alimi ochuluka m’chigawochi.

Mkulu wa kuofesiyi a Isaac Chipeta auza Radio Maria Malawi kuti padakali pano ofesiyi yakwanitsa kuthira mankhwala ophera tizilomboti m’ma ekala okwana 5, 250 mwa ma ekala okwana 17, 500 omwe akhudzidwa ndi tizilomboti. “ma ekala amene akhudzidwa ndi okwana 17,500 mmaboma amenewa a machinga, mangochi, balaka ndi zomba. Kudzera mu unduna wa za ulimi talandira ma litre 250 a mankhwala a cypermethrin ndipo padakli pano takwanitsa kuthira mankhwalawa ma ekala okwana 5, 250 koma ntchitoyi ikupitilirabe.

Iwo ati vuto limene lilipo ndi la kathiridwe ka mankhwalawa choncho apempha alimi kuti atsate njira zoyenera zothilira mankhwalawa kuti tizilomboti tife.

“Alimi ambiri akukanika kuthira bwino mankhwalawa. Akuyenera azithira pa mchombo penipeni pa chimanga paja kapena amati pa funnel ndipo awonetsetse kuti mankhwalawo akhudzana ndi chilombocho chifukwa akangowaza sizikumafa ayi,” anatero a Chipeta.

Poyankhapo pa nkhaniyi nduna yoona za ulimi, ulimi wa nthilira ndi chitukuko cha madzi Dr. George Chaponda, anati zilombozi zikhudza kakololedwe ka anthu mdziko muno koma alimi asadere nkhawa kaamba koti boma latumiza chitsanzo cha zilombodzi mdziko la Togo kuti akazipime ndi kupeza mankhwala ake eni eni.

“Tatumiza sample ya tizilombo timeneti mdziko la Togo kuti akatiyeze ndi kupeza mankhwala ake enieni chifukwa amene tikugwiritsa panowa saukgwira ntchito kwenikweni,” anatero Dr. Chaponda.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>