Bungwe la Parent and Child Health Initiative (PACHI) lapempha amayi kuti azipita ku chipatala msanga akakhala oyembekezera pofuna kuchepetsa imfa zokudza kaamba ka uchembere.
Mkulu woona za ma pologalamu ku bungweli mayi Laura Munthali ndi omwe anena izi mu mzinda wa Zomba pa mwambo wokhazikitsa komiti yomwe iziwona za uchembere wabwino m’bomalo yomwe ikutchedwa Bwalo Lathu.
Iwo apemphanso makolo kuti azilangiza ana awo kuti apewe kuchita chiwerewere kuti asatenge pathupi adakali achichepere kaamba koti imfa zambiri za uchembere zimakhala za atsikana omwe sanakwanitse zaka 18zakubadwa.
Polankhulanso pa msonkhanowu mfumu yaikuluChikowiya m’bomaliyapempha makolo kuti asamalekelere ana awo kupita ku malo achisangalaro usiku kuwopa kuti angamachiteko zinthu zosayenera