Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu Atatu Amangidwa Kamba Koba Katundu ku CADECOM

$
0
0

Apolisi m’boma la Balaka agwira anthu atatu omwe akuwaganizira kuti ndi amene akukhudzidwa ndi mulandu wakuba ku malo a mpingo wakatolika a CADECOM ku Ulongwe ndi ku malo a zaulimi wa nthilira a Nankhono Irrigation Schemem’bomalo.

Wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Constable Gerald Sumaili wati padakalipano apolisi-wa akwanitsanso kupeza wina mwakatundu yemwe anabedwa m’malowa, yemwe ndi monga makina opangira mphamvu za magetsi kuchokera ku dzuwa a Solarokwanira khumi ndi amodzi(11), njinga yamoto komanso makina awiri opopela madzi. Katundu-yu ndi wa ndalama zokwanira 11 Million Kwacha.

Anthu omwe ali m’manja mwa apolisi-wo ndi a FabianoChisale a zaka 42 zakubadwa, a Peter Chiwaya a zaka 37 zakubadwa kudzanso a Gift Kadali a zaka 29zakubadwa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>