Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

OPHUNZIRA AM'SUKULU ZASEKONDALE APINDULA NDI DSTV

$
0
0

Kampani ya Multi Choice Malawi yati ophunzira a m’sukulu zasekondale zomwe sizaboma tsopano ali ndi mwayi opindula nawo kudzera ku mapologalamu awulele othandiza pamaphunziro omwe amawonetsedwa pa kanema ya DSTV.

Polankhula pambuyo popereka zipangizo zatsopano za DSTV m’sukulu zasekondale za St Micheals Girls ndi Majuni m'boma la Mangochi mkulu wowona za malonda ku kampaniyi a Chimwemwe Nyirenda ati kampaniyi ndiyokonzeka kuyika ndondomekoyi m'sukulu za sekondale zomwe sizaboma zomwe zili kale ndi DSTV. Malinga ndi a Nyirenda sukulu 41 zasekondale za boma ndi zomwe zikupindula ndi ndondomekoyi mdziko muno.

‘’Chikhazikitsire ndondomekoyi mchaka cha 2008 tawona kusintha kwambiri chifukwa pano chiwerengero cha ophunzira omwe akuchita bwino pa maphunziro awo chikumakhala chokwera msukulu zimenezi’’ anatero a Nyirenda.

A Nyirenda ati chaka chino kampaniyi iwonjezera sukulu zina zisanu zasekondale pa mndanda wa sukulu zomwe zikupindula ndi ndondomekoyi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>