Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

ANTHU AKU CHIKHWAWA AKUKAKAMIZA MFUMU YAWO KUTI ITULE PANSI UDINDO

$
0
0

Anthu a mdera la mfumu Ngowe m’boma la Chikhwawa awopseza kuti achita ziwawa ngati  boma siliwathandiza pa nkangano wawo ndi mfumu Ngowe yomwe ati yakhala ikugulitsa minda yawo kwa anthu andale komanso anthu abizinezi.

Anthuwa anakapereka chikalata chokhuza madandaulo awo kwa bwana nkubwa wa bomali. M’modzi mwa anthu okhudzidwawo m’busa Lapson Mbewe wati akufuna kuti boma lichotse mfumu Ngowe pa udindo chifukwa ataya nayo chikhulupiriro.

‘’Ndi zomvetsa chisoni kuti nkhaniyi ikupitirirabe ngakhale bwalo la milandu linapereka kale chigamulo kuti anthu omwe anagula malowa asiye kulowerera malo athu’’ anatero Mbusa Mbewe.

Anthuwa apereka masiku 21 kuti boma liyankhe madandaulo awowa maka powachotsera mfumuyi kamba koti ikuphwanya ufulu wawo. Polankhula atalandirachi mkulu oyendetsa ntchito ku khonsoloyi a Noel Dakamawu ati apereka chikalatachi mmanja mwa anthu oyenera omwe angathandize pankhaniyi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>