Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Ma Episkopi Apempha Mayiko Athandize Anthu a Njala Mdziko la South Sudan

$
0
0

Ma episkopi a mpingo wa katolika mdziko la South Sudan apempha maiko akufuna kwabwino kuti athandize anthu amene akuvutika ndi njala mdzikolo.

Malinga ndi chikalata chomwe ma episkopiwa alemba, apemphanso boma la dzikolo kuti achite nalo zokambirana za mtendere ndi cholinga chothetsa nkhondo ya pa chiweniweni yomwe ikuchitika mdzikolo yomwe ati ikuzunzitsa anthu ambiri osalakwa.

Malipoti a Catholic News Agency (CNA) ati mu chikalatachi ma episkopiwa akufuna kukumana ndi mtsogoleri wa dzikolo kuphatikizapo onse amene akukhudzidwa ndi nkhaniyi.

Iwo ati akukhulupilira njala yomwe ili mdzikolo yomwe yakhudza anthu oposa 100 thousand ndi ya dala ndipo ikanatha kupeweka.

Dziko la South Sudan lakhala lili pa nkhondo ya pa chiweniweni kuyambira m’mwezi wa December 2013 pamene ziwawa zinayamba ku likulu la dzikolo ku Juba ndi kufalikira mdziko lonse.

Nkhondoyi ndi ya pakati pa anthu otsatira mtsogoleri wa dzikolo ndi ena otsatira yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dzikolo ndipo ikukhudza kwambiri mitundu ya wanthu.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875