Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Monsinyo Tamani Apempha a Malawi Azithandizana pa Nkhani ya Njala

$
0
0

Arkidayosizi ya Blantyre ya mpingo wakatolika yalimbikitsa a Malawi kuti azithandizana okhaokha pamene anthu ena akhudzidwa ndi vuto la njala.

Vicar General wa Arkidayosiziyi Monsinyo Boniface Tamani ndi omwe alankhula izi ku parishi ya Mwanga m’boma la Phalombe pa mwambo wokhazikitsa ndondomeko yopereka chakudya kwa anthu omwe akhudzidwa ndi vuto la njala kudzera mu thandizo lochokera kwa mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapereka kuno ku Malawi.

Monsinyo Tamani wati a Malawi aphunzire kuthandizana okhaokha ndi zochepa zomwe alina nazo potengera chitsanzo cha zomwe mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu wachita powonetsa kukhudzidwa kwake ndi anthu ovutika.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>