Anthu okwana 26 sauzande a m’dziko la Iraq athawa kum’mvuma kwa mzinda wa Mosul pa masiku okwana khumi 10 potsatira kumenyana komwe kunabuka pakati pa asilikali a dzikolo ndi zigawenga za Islamic State zomwe zakhala zikulamulira mbali ina ya mzindawu.
Malingana ndi malipoti a News24, chiwerengero cha anthu amene akwanitsa kuthawa ndi chochepa potengera anthu okwana 750 sauzande amene akuluakulu ena akukhulupilira kuti akukhala mokakamizidwa m’manja mwa zigawengazi.
Zigawenga za Islamic State (IS) zakhala zikulamulira kumpoto ndi kum’mvuma kwa mzinda wa Baghdad kuyambira mu chaka cha 2014 ndipo asilikali a dziko la Iraq mothandizana ndi asilikali aku America akwanitsa kulanda mbali yaikulu ya mzindawo.