Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Boma Lipempha Anthu Asamalire Nkhalango ya Dzalanyama

$
0
0

Boma lapempha anthu omwe amakhala malo ozungulira nkhalango ya Dzalanyama mu mzinda wa Lilongwe kuti asunge mitengo ya mu nkhalangoyi ndi cholinga chofuna kuchepetsa vuto la kuvuta kwa madzi mu mzindawo.

Mlembi wamkulu wa boma a Llyod Muhara ndi omwe alankhula izi ndi atolankhani a Malawi News Agency MANA pa mwambo wobzala mitengo ku nkhalangoyi ndipo ati nkhalangoyi imathandiza kuti madzi mu mzindawu asamavute choncho ikuyenera kusamalidwa.

Iwo anayamikira asilikali ngakhalenso mafumu potengapo mbali yoonetsetsa kuti nkhalangoyi ikutetezedwa.

Polankhulapo pa mwambowu wapampando wa kampani ya Lilongwe Water Board a Kayisi Sadala analimbikitsa boma ndi mabungwe kuti apitilize kudzipereka pa nkhani yobzala mitengo mu nkhalango za mdziko muno chaka ndi chaka.

Iwo anatsindika kufunika kowonjezera mitengo mu nkhalangozi pa nyengo ino yobzala mitengo kaamba koti  zithandiza kupewa ngozi zogwa mwadzidzidzi.

Ofesi ya pulezidenti ndi nduna mogwirizana ndi kampani Lilongwe Water Board komanso nthambi yowona za nkhalango yapereka mitengo yokwana 34 sauzande yomwe ikuyenera kubzalidwa mu nkhalango za mdziko muno chaka chino.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875