Bwalo lalikulu lamilandu la apilo mdziko la Egypt lapeza osalakwa yemwe anali mtsogoleri wakale wa dzikolo a Hosni Mubarak pa mlandu ozunza ndi kupha anthu mazanamazana pa ziwonetsero zomwe zinachitika mdzikolo mu chaka cha 2011.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC chigamulochi chadza a Mubarak atakamang’ana ku bwalo lalikulu pa chigamulo chomwe analandira mu chaka cha 2012 chokakhala ku ndende moyo wao onse kaamba kopezeka olakwa pa mlanduwu.
Koma boma la mtsogoleri wa dzikolo a Abdul Fattah al-Sisi ati silimafuna kutulutsa a Mubarak mu ndende powopa zotsatira zosayera kuchokera ku mzika za dzikolo.