Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Wapolisi Wosowa Wapezeka Atafa Atazimangilira

$
0
0

Wapolisi yemwe anasowa ku Police College mu mzinda wa Zomba wapezeka atafa atadzimangilira ku minda ya ku Chancellor College mu mzindawo.

Mkulu wofalitsa nkhani mchigawo cha kummawa cha dziko lino InspectorJoseph Saukawatsimikiza za kupezeka kwa thupi la malemuyu, Assistant SupretendentDickson Kaipa Gamayemwe anasowa pa 28mwezi watha.

Iwo ati patsiku losowali Assistant Supretendent Gamaanalemba kalata yoti akufuna kuzipha. Mneneri wa apolisiyu Inspector Saukawachenjeza anthu kuti akakhala ndi mavuto asamathamangire kudzipha ndipo mmalo mwake aziwuza anthu ena za mavuto awo kuti awathandize maganizo.

Assistant SupretendentGamayemwe amagwira ntchito kuPolice Collegemu mzinda waZombakuBand Sectionamwalira ali ndi zaka57zakubadwa ndipo asiya mkazi ndi ana atatu.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>