Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Patron Akondwera ndi Bungwe la YCS mu Arkidayosizi ya Lilongwe

$
0
0

Patron wa bungwe la ophunzira a chikatolika msukulu za sekondale la Young Christian Students (YCS) a Phillip Nsinawana Mwale ayamikira momwe ntchito za bungweli zikuyendera mu arkidayosizi ya Lilongwe.

A Mwale omwe ndi a mu dayosizi ya Zomba anena izi ku sukulu ya sekondale ya Bwaila pa mwambo umene sukulu za sekondale mu arkidayosiziyi  zimakalembetsa kukhala ma membala a bungweli.

Iwo ati kufika kwa sukulu zosiyanasiyana ku mwambowu kwawonetseratu poyera chidwi chomwe ophunzira ali nacho mu bungweli.

Faith Kamanga, wophunzira wa pa sukulu ya sekondale ya Chifuniro anati bungweli lithandiza ophunzirawa kupewa makhalidwe oyipa omwe angawachititse kuiwala ziphunzitso za mpingo wa katolika.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>