Amayi ochokera m’mipingo yosiyanasiyana m’dziko muno awapempha kuti azikonda kutanganidwa ndi zinthu zomwe zingathandize pa chitukuko cha miyoyo yawo ndi dziko lino.
Mayi Trizer Masauli omwe amatsogolera mwambo wa mapemphero a amayi ochokera m’mipingo yosiyanasiyana ya chikhristu, womwe wachitika pa 11 March 2017 m’boma la Mangochi ndi amene anena izi pakutha pa mwambo-wu.
Iwo ati nthawi yakwana yoti amayi achikhristu adzionetsa zitsanzo zabwino kuti mbiri yawo idzikhala yowala nthawi zonse.
Ku mwambo-wu kunafika amayi ochokera m’mpingo yoposera khumi ya chikhristu m’bomali.