Amayi a chikatolika mu arkidayosizi ya Blantyre awapempha kuti azamitse moyo wawo wa mapemphero ngati njira imodzi yosinkhasinkha moyenera masautso a ambuye yesu khristu.
Mlembi wa za utumiki mu dayosizi ya Mangochi bambo Steven Kamanga ndi omwe alankhula izi ku Limbe Cathedral mu arkidayosizi ya Blantyre pambuyo pa m’bindikiro wa tsiku limodzi omwe amayi a mu arkidayosiziyi anakonza ndi cholinga choti azamitse moyo wawo wa mapemphero.
Iwo ati m’bindikirowu ndi ofunika kwambiri kwa amayiwa maka posinkhasinkha za chikhristu chenicheni chofumira mu mtima.
Pamenepa iwo anati kuti zimenezi zitheke amayiwa akuyenera kulimbikira moyo wa masakramenti, mapemphero komanso ubale pakati pawo.