Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Maepiskopi Mdziko la USA ati Miyoyo ya Anthu Osauka ili pa Chiopsezo

$
0
0

Maepiskopi a mpingo wa katolika mdziko la United States of America ati miyoyo ya anthu ovutika mdzikolo ili pa chiopsezo potsatira ndondomeko yatsopano ya zaumoyo yomwe yakhazikitsidwa mdzikolo.

Malinga ndi chikalata chomwe chasinidwa ndi episkopi wa dayosizi ya VeniceAmbuyeFrank J Dewane kupita ku nyumba ya mtsogoleli wa dzikolo, ma episkopiwa ati pamene ndondomekoyi ikupereka chitetezo ku miyoyo ya anthu ikuperekanso chipsyinjo kwa anthu osauka ndi ovutika choncho ikuyenera kuganiziridwa bwino.

Chikalatachi chati ndondomekoyi izilepheretsa anthu ovutika kupeza thandizo la mankhwala zimene ati zikungoonetselatu kuti boma la dzikolo silikuganizila miyoyo ya anthu ovutika komanso osauka.

Pamenepa chikalatachi chapempha boma la United States kuti liganidze bwino za ndondomekoyi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>