Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Ambuye Msusa Apempha Amayi Azipereke Potukula Uzimu

$
0
0

Arkiepiskopi wa arkidayosizi ya mpingo wa katolika ya Blantyre Ambuye  Thomas Luke Msusa walimbikitsa amayi mu arkidayisizi-yi kuti azipeleke potukula uzimu pakati pa anthu.

Ambuye Msusa apeleka pempholi ku Nantipwiri Pastoral Center m’boma la Thyolo potsekela msonkhano wa sabata imodzi wa atsogoleri a bungwe la a mai la Catholic Women Organisation (CWO) ochokera m’ma dinale onse a mu arkidayosizi-yi. Iwo ati mpingo umayamika kwambiri ntchito za a mai pa chipembedzo ndipo akuyenera kudzindikira kuti ntchito imeneyi ndiyofunikira potukula umoyo wauzimu pakati pa anthu.

Poyankhulapo mlembi wamkulu owona za utumiki mu arkidayosizi yaBlantyrebamboAlfred Chaimaanati nthambi yawo yoona zautumiki yakonza maphunziro apamwamba ofuna kusula atsogoleriwa kuti atenge nawo mbali poyendetsa mpingo. Pothilapo ndemanga mai Lucy Vokhiwa omwe ndi wapampando wa bungwe la amai mu arkidayosizi-yi, ayamikira arkidayosiziyi kaamba ka maphunzirowa ponena kuti ziwathandiza kudziwa zoyenera kuchita pa utsogoleri wawo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>