Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

NDUNA YA ZA UMOYO YATI KUNYALANYAZA KWA OGWIRA NTCHITO KUNAWONGETSA MATUPI A ANTHU PACHIPATALA CHA K

$
0
0

Nduna ya za umoyo mayi Catherine Gotani Hara, ati kunyalanyaza kwa akulu akulu apachipatala cha Kamuzu Central mu mzinda wa Lilongwe ndi komwe kunachititsa kuti matupi ochuluka a anthu awonongeke ku nyumba ya chisoni yapachipatalachi.

Mayi Hara, alankhula izi lachiwiri pa msonkhano wa atolankhani womwe pulezidenti wadziko lino Dr Joyce Banda anachititsa mumzinda wa Lilongwe.

Zipinda zitatu zosungiramo matupi anthu kuti asawonongeke zinawonongeka pachipatalacho zomwe zinachititsa kuti nyumba ya chisoni yapachipatalacho ayitseke.

Malinga ndi ndunayi, mwezi wa December chaka chatha m’modzi mwa ogwira pachipatalachi anadziwitsa woyendetsa ntchito zachipatalacho a Mable Chinkhata kuti matupi omwe anadzadza mnyumba yachisoniyo awachotse ndikukawakwirira koma ati izi sizinachitike.

Mayi Hara anati a Chinkhata anasankha kupita ku tchuthi asanakonze za vutoli ndipo anati munthu yemwenso anamusiyira ntchitoyi sanalabadirenso za vutoli.

Malinga ndi mayi Hara chipatalacho chinapatsidwa ndalama zomwe zikanatha kugwiritsidwa ntchito pokonzera zipangizo zomwe zinawonongekazo.

“Pa 11 february analandira ndalama zokwana 33 miliyoni kwacha komanso zina 89 miliyoni kwacha pa ndalama zonsezi akanatha kukonzetsera zipangizo zowonongekazo” anatero a Hara.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko