Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

92 BILIYONI KWACHA INABEDWA MCHAKA CHA 2010-JB

$
0
0

Mtsogoleri wa dziko lino Dr Joyce Banda wati kafukufuku wapeza kuti ndalama pafupifupi 92 biliyoni kwacha za boma zinasowa m'chaka cha 2010 mu ulamuliro wachipani cha Democratic Progressive (DPP).

Pulezidenti Banda wanena izi lipoti la kafukufuku wa kubedwa kwa ndalama za boma yemwe achita akatswiri amdziko la Britain litapeza kuti ndalama zokwana 13 biliyoni kwacha zinasakazidwa kuchokera pomwe anayamba kulamulira dziko lino.

Polankhula pa msonkhano wa atolankhani mumzinda wa Lilongwe lachiwiri, Dr Joyce Banda anati anthu akuyeneranso kudziwa chomwe chinachitika kuti ndalama pafupifupi 92 biliyoni kwacha zisowe mchaka cha 2010.

‘’ Pali lipoti la 2010 enafe kulibe kuphatikizapo nduna zambiri zili apazi kunalibe lomwe linapeza kuti ndalama zokwana 92 biliyoni zinabedwa’’ anatero mayi Banda.

Pothirirapo ndemanga pa za mayina omwe sakutchulidwa mu lipoti lakubedwa kwa ndalama lomwe laperekedwa kunyumba ya malamulo posachedwapa, Pulezidenti Banda anati alinso ndi chidwi chofuna kudziwa mayina anthu omwe sanatchulidwe mu lipotili.

‘’ Tonse tili ndi chidwi chofuna kudziwa mayina anthu amenewa”  anatero Pulezidenti Banda.  

Mtsogoleri wadziko linoyu wati nyumba ya malamulo ikambirane pa nkhani ya kubedwa kwa ndalama zonse kuyambira 92 biliyoni kwacha komanso 13 biliyoni kwacha. Dr Banda anati wayitanitsa akatswiri akawuniwuni amdziko la Britain omwe amachita kafukufuku wa kubedwa kwa ndalamazi kuti akalongosolere nyumba ya malamulo za lipoti komanso kusapezeka kwa mayina mulipotilo.

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>