Bwalo la milandu la Mkukula Magistrate mu mzinda wa Lilongwe lalamula bambo wina kuti akakhale ku ndende kwa zaka zisanu ndi zitatu (8) ndikukagwira ntchito yakalavula gaga atamupeza olakwa pa mlandu ogwilira asungwana awiri omwe ndi azaka zosapyola 16.
Wofalitsa nkhani pa polisi ya Kanengo mu mzinda wa Lilongwe constable Salome Chibwana wati bambo-yu Damington Langton wa zaka 46 wa mdera la mfumu yaikulu Chitukula m’boma la Lilongwe anagwililira asungwanawa omwe m’modzi ndi mwana wake womupeza ndipo wina ndi mzake wa mwanayo.
Mneneri wa apolisiyu wapempha amayi onse kuti azikhala osamala pamene akusiya ana awo pakhomo ndi a bambo.