Yemwe anali mtsogoleri pothetsa mchitidwe wa tsankho mdziko la South Africa a Ahmed Kathrada wamwalira.
Malipoti a wailesi ya BBC ati a Kathrada amwalira ali ndi zaka 87 zakubadwa, atadwala kwa kanthawi kochepa pomwe anawachita opaleshoni ya mu ubongo.
A Kathrada omwe anali mgulu limodzi ndi a Nelson Mandela pomwe ankamenyera ufulu wa anthu pothetsa mchitidwe wa tsankho mdzikolo, anasungidwa m’ndende kwa zaka 26 ndipo anawatulutsa mchaka cha 1989.
Malemuyu anasiya kukhala phungu nyumba ya malamulo m’chaka cha 1999 komabe anali wamphamvu pandale ndipo posachedwapa anauza mtsogoleri wa dzikoli a Jacob Zuma kuti atule pansi udindo wawo.