Khonsolo ya mzinda wa Zomba yakhazikitsa ubale ndi gulu la asilikali a nkhondo aku Changalume Barracks.
Polankhula pa mwambo wosayinilana ubale-wu omwe unachitikira ku likulu la khonsolo-yi, Mayor wa mzinda wa Zomba khansala Meria Likoswe Douglas wati ubalewu upeleka mwayi kwa asilikali aku Changalume kuti akhale mfulu mu mzinda wa Zomba.
Iwo ati asilikaliwa akhala akupeleka chitetezo kwa anthu amu mzinda-wo.
Polankhulanso pa mwambo-wu wachiwiri kwa mkulu wa asilikali aku Changalume Barracks, Major Raphael M’bobo Phiri wati ubale umene-wu uchititsa kuti asilikaliwa adzigwira ntchito zawo zosiyanasiyana mu mzindawo.
Iwo ati asilikali-wa aziguba perete mu mzinda wa Zomba kamodzi pa chaka.