Boma lati bungwe la Leadership for Environment and Development in Southern and Eastern Africa (LEAD-SEA) lakwaniritsa ntchito yake yolimbikitsa ndi kubwezeretsa chilengedwe mchigwa cha Nyanja ya Chilwa pansi pa ndondomeko ya Lake Chilwa Basin Climate Change Adaptation Program (LCBCCAP).
Mmodzi mwa akuluakulu ku unduna wa za chilengedwe magetsi ndi migodi, a Yanira Ntupanyamandi omwe alankhula izi pamwambo omwe bungwe la LEAD linakonza ndi cholinga chofuna kufotokozera anthu komanso boma ntchito zomwe lakhala likugwira zobwezeretsa chilengedwe mchigwa cha Nyanja ya Chilwa zomwe ati zafika kumapeto tsopano.
A Ntupanyamaati dziko la Malawi, lapindula kwambiri ndi bungweli chifukwa m’madera ambiri omwe bungweli lakhala likugwira ntchito zake, anthu ndi odzidalira komanso chilengedwe chathandiza kuti mitsinje yambiri yomwe inaphwera iyambenso kukhala ndi madzi chifukwa cha ndondomeko yomwe bungweli lakhala likutsatira.
Polankhulapo mkulu wa bungwe la LEAD, ProffesorSostenChiothawati ntchito yobwezeretsa chilengedwe yakhala yopambana kwambiri pomwe akwanitsa kudzala mitengo yochuluka ngakhale kuti akumana ndi zovuta zina.