Bungwe la achinyamata la Youth InitiativeforCommunity Development(YICOD) lati atolankhani ali ndi udindo wofalitsa nkhani zokhudza momwe ndondomeko ya ndalama za m’thumba la sukulu za boma la School Improvement Grant likugwirira ntchito zake potukula maphunziro mdziko muno.
Mkulu wa bungweli a Andrew Bwanali alankhula izi pambuyo pa ulendo omwe bungweli linakonzera atolankhani wokayendera sukulu za mdera la mfumu yaikulu Kasumbu m’boma la Dedza.
Iwo ati pozindikira momwe bungweli likugwilira ntchito zake, anthu akuyenera kuti azidziwa momwe thandizo la ndalamali likugwilira ntchito kudzera mwa atolankhani.