Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu Azisunga Agalu Osaposera Atatu Kuti Apewe Chiwewe

$
0
0

Matenda a chiwewe akuti angathe ngati anthu atamakhala ndi agalu osachepera atatu m’makomo mwawo.

M’modzi mwa akuluakulu kuofesi yoona za nyama ya Vetenale ku Thondwe m’boma la Zomba a William Masangano anena izi polankhula ndi mtolankhani wathu , amene amafuna kudziwa momwe ofesi yawo ikudzipelekera pa ntchito yolimbana ndi matenda-wa m’bomalo.

A Masangano ati anthu amene ali ndi nambala ya agalu oyenera amatha kukwanitsa kupeleka chisamaliro chokwanira kwa agalu omwe ali nawo , ndipo izi zimathandiza kuti agalu-wo asamangoyenda-yenda mwachisawawa ndi kumanka naluma anthu pofalitsa matenda a chiwewe.

“Munthu wina aliyense asakhale ndi agalu opitilira atatu. Ndipo ndi njala imene ilipo chaka chinoyi, kuti munthu akapeze chakudya choti adye iyeyo ndiye apezenso china cha agalu zimene ndi zodula. Ndipo panopa ndi mating period ndiye agalu amaswa kwambiri mwina ana 15 pakamodzi,” anatero a Masangano.

Iwo ati akugwira ntchito mothandizana ndi mafumu m’madera ozungulira Thondwe kuti athetse matenda achiwewe wa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>