Bwalo la milandu m’dziko la France lalamula mafumu awiri a mizinda ina ya m’dziko la Rwanda kuti akakhale kundende moyo wawo wonse kamba kokhudzidwa ndi mulandu wakuphedwa kwa anthu ochuluka m’chaka cha 1994.
Mafumu-wa a Tito Barahira a zaka 65 zakubadwa ndinso a Octaven Ngezi a zaka 58 zakubadwa awapezeka olakwa pa mulandu wotengapo gawo lalikulu pa imfa ya anthu 2 Sauzandeamtundu wa chi Tutsiomwe pamthawiyo mkuti anali akubisala patchalitchi lina mu m’dzinda wa Kabarondom’dzikomo.
Pafupifupi anthu 8 Thousand a mtundu wa chi Tutsianaphedwa ndi anthu a mtundu wa chi Hutunthawi yomwe mitunduyi inali kusemphana maganizo muzochitika zina potsatira imfa ya yemwe anali m’tsogoleri wa dzikolo Juvenal Habyarimanaamene anaphedwa ali mu ndege ndi anthu ena osadziwika.