Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Apempha Anthu Asamalire Anthu Othawa Kwawo

$
0
0

M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Fransisko wati mayiko akuyenera kusamalira bwino anthu omwe akumafika m’mayiko awo kamba kothawa nkhondo ndi zipolowe zomwe zikuchitika m’mayiko awo.

Papa Francisco walankhula izi pomwe amalandira maanja atatu omwe afika ku likulu la mpingo-wu ku Vatican, kamba kothawa nkhondo ya pa chiweniweni yomwe ikuchitika m’dziko la Syria.

Limodzi mwa mabanjawa ndi la chisilamu. Padakalipano mabanjawa awapatsa malo oti azikhala mwabata ndi mtendere.

M’tsogoleri wa mpingo wakatolikayu  anakhadzikitsa ntchito yothandiza anthu-wa pa 6 September 2015 pomwe anali kuchita mapemphero mthenga wa m’njelo.

Mwa zina pa tsikuli Papa walimbikitsa akhristu a mpingo wakatolika kuti akhale patsogolo pothandiza anthu-wa kamba koti amakhala ali pa mavuto akulu okhudza moyo wawo.

Padakalipano bungwe la Community of Saint Egidio ndi lomwe linadzipeleka pothandiza pa ntchito-yi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875