M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati ntchito yolimbana ndi m’chitidwe wozembetsa anthu itha kukhala yopanda pake ngati mayiko sazichilimika pa ntchito yolimbana ndi mchitidwe-wu.
Papa walankhula izi kudzera mu uthenga wake umene wapeleka mwa padera, kwa nthumwi za bungwe la Organisation for Security and Cooperation in Europezomwe zimachita zokambilana nawo mu m’dzinda wa Vienna m’dziko la Italy, zokhudza njira zothanilana ndi mchitidwewu m’mayiko a ku Ulaya.
Zokambilanazi ndi za nambala 17 kuchitika pakati pa bungweli.
Mu uthengawu papa anatsindika ponena kuti m’chitidwe wozembetsa anthu ndi woyipa kwambiri, kamba koti ukukhudzanso kwambiri amayi ndi ana omwe akunzunzika mu njira zosiyanasiyana nchoncho mayiko sakuyenera kungokhala koma kuonetsetsa kuti akulimbana ndi m’chitidwe-wu ndi kuthana ndi onse omwe akulimbikitsa mchitidwe woyipa-wu.