Anthumakumi awiri (20)afa boti lomwe anakwera litaombana ndi linzake ndi kumira mu m’tsinje wina m’dziko la Myanmar.
Malingana ndi malipoti a News 24 anthu amene anali mu botili ndi oti anali akuchokera ku mwambo wa ukwati ku dela lina ndipo onse analipo 60.
Malipoti-wo ati mwa anthu omwe afawo 16ndi amayi ndipo anayiwo ndi amuna.
Ngozi za pamadzi akuti zimakonda kuchitikachitika mdzikomo kamba koti anthu ambri amakonda kugwilitsa ntchito maulendo a pamadzi.