Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Apolisi Akusakasaka Dalaivala Wina Kaamba Kopha Munthu, Kuthawa

$
0
0

Apolisi m’boma la m’boma laDowaakufunafuna dalaivala wa galimoto ina kamba komuganizira kuti anagunda ndi kupha a Akimu Dayison a zaka 38zakubadwa m’bomalo.

Ofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Sergeant Richard Kaponda ngoziyi yachitika usiku wapa 8 mwezi uno pomwe dalaivalayu anaomba bambo-yu mu msewu Salima kupita ku Lilongwe. Ngozi-yi inachitikira m’mudzi mwa Sole m’bomalo.

A Kaponda ati dalayivala wa galimoto lomwe linaomba ndi kupha malemu-wa atachita ngoziyo akuti anathawa ndipo apolisi akhadzikitsa ntchito yosakasaka ndalaivala-yu.

Malemu-yi Akimu Dayson anali wochokera m’mudzi mwa Singo m’dera la mfumu yayikulu Mkukula m’boma lomwelo la Dowa.

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>