Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Akuyembekezeka Kuyendera Dziko la Egypt

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisko akuyembekezeka kukayendera dziko la Egypt sabata ikudzayi.

Malipoti a wayilesi ya Vatican ati mwazina Papa akayendera sukulu ya maphunziro a chisilamu ya Al-Azhar ndipo mtsogoleri wa mpingo wa Orthodox, Patriarch Bartholomew komanso mtsogoleri wa mpingo wa Coptic, Papa Tawadrows wachiwiri akuyembekeza kukhala ndi Papa Francisko pa ulendowu.

Papa Francisco komanso Patriarch Bartholomew ayitanidwa ndi sukulu ya chipembedzo cha chisilamuyi kuti akakhale nawo pa msokhano wokumbukira mtendere pa dziko lonse womwe uchitikire mdzikolo.

Pa ulendo wakewu, pa 28 komanso 29 April, Papa akuyembekezeka kukakumana ndi mtsogoleri wa dzikolo a Abdul Fattah Al-Sisi komanso kutsogolera mwambo wa nsembe ya misa ku tchalitchi lina la mpingo wa katolika mdzikolo.

Ulendo wa Papa mdziko la Egypt ukudza pasanathe mwezi pamene zigawenga za Islamic State zinachita chiwembu pa tchalitchi ziwiri za mpingo wa Coptic chomwe chinapha anthu 45 ndi kuvulaza ena ambiri.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>