Nduna ya za chitetezo ndi mkulu wa asilikali m’dziko la Afghanstan yatula pansi ma udindo wake, kaamba ka kuphedwa kwa asilikali a dzikolo ndi gulu la za uchifwamba la ma Taliban.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC chiwembuchi chinachitika lachisanu pa malo a asilikali kumpoto kwa dzikolo pomwe anthu omwe anavala ngati asilikali anachitila chiwembu asilikaliwa pa nthawi yomwe amachokera ku mzikiti.
Padakali pano chiwerengero cha asilikali omwe afa pa chiwembuchi sichikudziwika ngakhale malipoti osatsimikizika akusonyeza kuti asilikali 165ndi omwe aphedwa.