Anthu akupitilira kufa mdziko la Venezuella pa chiwonetsero chosonyeza kusakondwa ndi utsogoleri wa a Nicholus Maduro chikupitilira ku likulu la dzikolo ku Caracus.
Malipoti a wailesi ya BBC ati anthu enanso atatu afa zomwe zafikitsa chiwerengerocho pa 24 chiyambireni ziwonetserozo zomwe zachitika kwa sabata zitatu tsopano ndipo anthu ambiri avulala modetsa nkhawa ndipo ali pakati pa moyo ndi imfa.
Chiwonetserochi chadza pomwe anthu mdzikolo akuti sakukondwa ndi m’mene boma la a Maduro likuyendetsera dzikolo.
Malipoti ena ati anthu omwe akuchititsa ziwonetselozi akufuna kuti mdzikomo muchitike zisankho ndipo kuti mtsogoleri wa dzikolo atule pansi udindo wake.