Unduna wa zaulimi, ulimi wa m’thilira ndi chitukuko cha madzi wapempha alimi kuti ayambe kugulitsa mbewu zawo boma likakhazikitsa mitengo ya m’bewu-zo ya mbewuzo.
M’modzi mwa akulu-akulu mu unduna-wu a Steven Mbewe ndi omwe alankhula izi m’dera la mfumu yaikulu Njolomole m’boma la Ntcheu pa chionetsero cha ulimi-wa soya.
Polankhulapo m’modzi mwa akuluakulu ku bungwe lowona za chitukuko mu mpingo wakatolika mu dayosizi ya Dedza la CADECOM a Aaron Kalamule ati Iwo ngati bungwe sangawaletse alimi kugulitsa mbewu zawo koma akuyenera kupeza misika yomwe angathandize kuti apeze phindu lokwanira pa zokolora zawo.