Bungwe la Maternity World Wide lapereka njinga za ambulance zokwana zisanu ndi zitatu 8 ku dera la gulupu Village Headman Kathebwe kudera la mfumu yaikulu Mwambo m’boma la Zomba.
Bungweli lachita izi pofuna kuchepetsa imfa za amayi ndi ana pa nthawi yochira komanso kuchepetsa vuto la mayendedwe pakati pa amayi oyembekezera a mderali kaamba koti chipatala cha Matiya chomwe amakapezako thandizo chili kutali.
M’mawu ake wachiwiri kwa mkulu wa nthambi ya za chitukuko mu dayosizi ya mpingo wakatolika ya Zomba a Raphael Yusuf athoza bungweli kamba ka thandizolo.
Iwo ati nthambi yawo pamodzi ndi bungweli apitiliza kuthandiza anthu a mdelari pa zitukuko zosiyanasiyana.
Polankhulapo m’modzi wa akuluakulu ochokera ku nthambi yoona zaumoyo m’boma la Zomba, yemwenso ndi mkulu woyang’anira uchembere wabwino m’bomalo mayi Seko Chisuwo ati ndi okondwa kaamba ka thandizoli ndipo apempha mabungwe ena m’dziko muno kuti atenge nawo mbali pa nkhani zaumoyo makamaka za uchembere wabwino.