Ophunzira achitsikana pa sukulu ya sekondale yoyendera ya Changali m’dera la a Senior Chief Chimwala m’boma la Mangochi apempha boma kudzera mu unduna wa za maphunziro kuti uwamangire Hostel pa sukulu-yi ndi cholinga choti azigonera pomwepo.
M’modzi mwa ophunzira pa sukulu-yi Halima Ali George wanena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi pamene inafika ku malo a sukuluyi.
Iye wati atsikana akulephera kuchita bwino pa maphunziro awo kamba koti madera emene amachokera ali kutali kwambiri ndi sukulu-yi zomwe zimapangitsa kuti asamachite bwino pa maphunziro awo mu njira zosiyanasiyana.
“Timakhala kutali ndiye munsewumu mvula imativuta ndipo tikamafika ku sukulu kuno timakhala otopa. Kuchokanso ku sukulu kono kukafika kunyumba timakafika mochedwa komanso otopa ndipo sitimakhala ndi nthawi yowerenga. Anthu ena anayamba kumapanga renti nyumba zoyandikira ku sukulu kuno koma amakumana ndi mavutonso ambiri monga kusowa ndiwo, chakudya komanso ndalama yolipira lenti. Zimenezi zimachititsa kuti azitengeka ndi anyamata akunyanja kumawapatsa nsomba kusinthanitsa ndi matupi awo pamapeto pake amatenga mimba ndi kusiya sukulu pena kutenganso matenda. Patakhala mahostel atsikana ndikumagonera konkuno ndiye kuti atsikana aphunzira bwino chifukwa azitetezedwa ndi aphunzitsi,” anatero Halima.
Polankhulanso m’modzi mwa aphunzitsi pa sukuluyi aRenex Matola Nyoni anagwilizana kwambiri ndi madandaulo a wophunzirayu. Iwo ati mavuto-wa sikutinso asiya mbali kamba koti pa sukuluyi palibenso nyumba zokwanira za aphunzitsi.
“Aphunzitsi ndi ochepa chifukwa nyumba palibe zokwanira zilipo zitatu zokha. Tikanakonda mabungwe ndi anthu akufuna kwabwino akanatithandiza chifukwa aphunzitsi ambiri amakhala kutali choncho amakanika kudzagwira ntchito yawo moyenera komanso munthawi yake,” anatero a Matola Nyoni.
Iwo ati zimakhala zodabwitsa kuti boma komanso mabungwe sachitapo kanthu ngakhale sukuluyi ili mbali mwa nsewu womwe umadutsidwa kwambiri (wochoka ku Mangochi kupita ku Liwonde)