Achinyamata a mpingo wakatolika mdziko muno ati akuyenera kukhala ndi mtima wa utumiki komanso akhale okonda kupemphera.
Episkopi wa dayosizi ya Mzuzu Ambuye John Ryan ndi omwe apereka pempholi ku St Denis Parish m’boma la Rumphi mu dayosizi-yi pambuyo pa mwambo wa chiyitanidwe.
Ambuye Ryan ati achinyamata nthawi zonse azikhala okonzeka pofalitsa uthenga wabwino komanso azipemphera molimba ngati akufuna zaulele zochokera kwa Mulungu.
“Tiyeni achinyamata nthawi zonse tifalitse za uthenga wabwino wa Yesu Khristu ndi kupemphera kuti Mulungu apitirize kutipatsa zaulele,” anatero Ambuye Ryan. Polankhula pa mwambowu mkulu waku ofesi yowona za mabungwe a utumiki wa apapa mdziko muno ya Pontifical Mission Societies (PMS) bambo Vincent Mwakhwawa ati achinyamata akuyenera kuganiza mofatsa ndi kuchita chisankho chabwino cha momwe angatumikilire Mulungu.
“Chimene tikufuna ife mu mpingo wakatolika ndi kuti achinyamata athu atenge nawo mbali mmayitanidwe osiyanasiyana amene alipo mu mpingo wathu,” anatero Bambo Mwakhwawa.
Mutu wa chaka chino wa tsiku la mayitanidwe unali wakuti “kutsogozedwa ndi mzimu wa utumiki.”