Wachiwiri kwa pulesident wa dziko la Iran a Eshaq Jahangiri watula pansi udindo wake ndipo kuti sayimananso pa udindo wa Pulezidenti patangotsala masiku ochepa kuti chisankho cha Pulezidenti wa dzikolo chichitike.
Malingana ndi malipoti a News 24 a Jahangiri ati amaliza ntchito yao ndipo amemeza mzika za dzikolo pa msonkhano omwe anali nawo kuti adzavotere a Hassan Ruhani omwe akudzapikisana nawo pa udindowu ndi cholinga choti apitirize ntchito yotukula dzikolo.
Ganizoli ladza patangodutsa tsiku limodzi meya wa mzinda wina wa dzikolo atalengezanso kuti sapikisana nawo pa chisankhochi.