M’tsogoleri wa dziko la South Sudan a Salva Kiir wachotsa paudindo wachiwiri wake a Riek Machar potsatira kumenyana kwa mphamvu komwe kunabuka pakati pa anthu otsatira atsogoleri-wa mu m’dzinda wa Jubam`dzikolo.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, Presidenti-yu wa sankha a Taban Deng Gaiyemwe analimkhala pakati wodzetsa mtendere m’dzikomo kukhala wachiwiri wake.
Padakalipano anthu otsatira wachiwiri kwa m’tsogoleri wa dzikolo amene wachotsedwa pa udindowu a Macharadzudzula zomwe m’tsogoleri wa dzikolo wachita pochotsa mkuluyi pa udindowu.
Iwo ati zomwe zachitikazi zisokoneza pangano la mtendere lomwe gulu loukira boma ndi asilikali a boma anasayinilana posachedwapa m’dzikomo