Anthu khumi (10) afa ndipo ena avulala anthu ena ataphulitsa mabomba awiri pa chipata cholowera kubwalo la ndege mu mzinda wa Mogadishum`dziko la Somalia.
Malinga ndi malipoti awailesi ya BBC, anthu omwe afawo ambiri ndi achitetezo chapamalopo. Atolankhani a m`dzikolo ati bomba loyamba linali la tinkenawo ndipo lina ati laphulika pafupi ndi khoma lalikulu ku bwalo la ndegero.
Pakadali pano gulu la zigawenga za Al-Shabaab lati ndilo lachita chiwembuchi.