Akulu-akulu oyang’anira ntchito za chitukuko m’ma WARD amu mzinda wa Zomba apempha khonsolo ya mzindawu kuti ikafuna kuchita ntchito zachitukuko iziyamba yauza akulu-akuluwo za momwe ntchitozo ziyendele.
Wachiwiri kwa mfumu ya mzinda wa Zomba khansala Davie Maunde anapereka pempholi pamkumano omwe bungwe la Bwalo Initiative linachititsa pofuna kuzindikiritsa makhansala komanso akulu-akulu a khonsoloyo za momwe angagwirile ntchito zachitukuko mogwirizana.
Khansala Maunde wayamikila bungwe la Bwalo Initiative kaamba koitanitsa mkumanowo komanso wapempha kuti ndalama zachitukuko zikabwera ku khonsoloyo zizigwira ntchito moyenera.
Mkulu woyang’anira mapulogalamu ku bungwe la Bwalo Initiative a Harry Phiri ati ndalama zomwe makhonsolo amagwiritsa pa zitukuko zosiyanasiyana ndi za aMalawi choncho ndi kofunika kuti anthu azidziwa momwe ndalamazo zikugwirila ntchito.