Bungwe la Malawi Union of the Blind latsutsa malipoti akuti mtsogoleri wa dziko lino Professor Peter Mutharika akumanyoza anthu osawona pa misonkhano ya ndale ngakhalenso ya boma.
Wapampando wa bungweli a Ezekiel Kumwenda alankhula izi poyankhapo pa zomwe anthu ena akunena kuti Professor Peter Mutharika akumanyoza anthu osawona.
Iwo ati akukhulupilira kuti m’malakhulidwe a mtsogoleri wa dziko linoyu akumatanthauza kusazindikira kapena kugwira ntchito mobwelera m’mbuyo osati kunyoza anthu osawona.