Ntchito za umoyo zayima pa chipatala cha boma la Mwanza kamba ka vuto la madzi pomwe odwala akutha masiku anayi asanasambe.
Malinga ndi zomwe Radio Maria yapeza, anthu odikirira odwala pachipatalacho akumakatunga madzi ku mtsinje wapafupi ndi chipatalacho zomwe zikuyika miyoyo ya anthuwa pachiwopsezo.
Ena mwa ogwira ntchito pa chipatalachi omwe anati tisawatchule afotokoza kuti zipinda zochirira ndi zopangira opareshoni odwala zasiya kugwira ntchito kamba kosowa madzi. Vutoli lachititsanso kuti zimbudzi zogwiritsa ntchito madzi zizipereka fungo loipa.
Bungwe lowona za madzi linadula madzi kamba koti chipatalacho chikulephera kupereka ngongole ya ndalama zoposa 4 Million kwacha kubungweri.