Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

MPINGO WA KATOLIKA KU MALAWI UWUNIKIRA ANTHU PA ZA CHISANKHO

$
0
0

Pamene kwangotsala miyezi iwiri kuti dziko la Malawi lichite zisankho zake zoyamba za patatu pa 20 May bungwe lampingo wakatolika la chilungamo ndi mtendere la CCJP latulutsa chikalata chomwe muli mfundo zothandiza anthu kuti azasankhe atsogoleri oyenera pa zisankhozi.

Chikalatachi chomwe mutu wake ndi Kulimbitsa masomphenya a kumene tilikupita: Kukonzekera chisankho chapatatu cha 2014 m’nyengo ya Lenti ndi Pasaka chikupereka mphamvu ndi kuunikira bwino udindo wa mzika za dziko lino panthawi ya zisankhozi.

Gawo loyamba la chikalatachi lasayinidwa ndi mlembi wamkulu wa bungwe la ma episkopi a kuno ku Malawi la Episcopal Conference of Malawi ECM bambo George Buleya komanso kuvomerezedwa ndi ma episkopi onse a mdziko muno.

Muchikalatachi bungweli lati dziko lino likufuna atsogoleri okhulupirika, anzeru, ophunzira komanso omwe ali mtima oganizira anthu oponderezedwa ndi ovutika omwe ali ku mudzi.

Bungweli lapemphanso akhristu mdziko muno kuti atengerepo mwayi mu nyengo ino ya Lenti komanso Pasaka ngati njira imodzi yokonzekelera ndi kudzipereka kwa Mulungu kuti athandize dziko lino kupeza mtsogoleri wa masomphenya.

“Nyengo ya Lenti ndi Pasaka tayambayi, kuyambira Tsiku la Phulusa, pa 5 March 2014, ndi nthawi ya mwai wapadera woti tipempherere ndikusinkhasinkha za atsogoleri omwe tingafune kusankha kuti ayendetse dziko lathu.Chisankho chapatatu chikubwerachi chidzachitika pamene dziko la Malawi lizidzakondwerera zaka 50 za ufulu wakudzilamulira ndi zaka 20 za ulamuliro wa zipani zambiri womwe udayamba m’chaka cha 1993. Tili pa mphambano yofunikira kwambiri pamene mwai waukulu wotenga nawo mbali posankha tsogolo la dziko lathu wagwanso m’manja mwathu” chatero chikalatacho.

Posachedwapa bungwe la ma Episikopi ampingowu linatulutsanso chikalata chopempha ndikuunikira anthu njira zoyenera zomwe angatsatire posankha atsogoleri aphindu ndi amasomphenya adziko lino.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>