Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Fransico Aikiza Mmapemphero Akhristu Omwe Aphewdwa Mdziko La Egypt

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse PAPA FRASISCO anaikiza mmapemphero akhristu a mpingo wina wachikhristuomwe avulazidwa komanso kuphedwa ndi a chiwembu mdziko la EGYPT.

Akhristuwa avulazidwa komanso kuphedwa mdera lina mdziko la Egypt pomwe anali pa ulendo wopita kumalo oyera kukapemphera. Mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu wapepesa Papa TAWADROS wa mpingo wa ORTHODOX komanso dziko lonse la Egypt. Pamepa papa wati ndiwokhudzidwa kwambiri ndi zamtopola zomwe anthu ena akuchitira mipingo yachikhristu mmaiko osiyanasiyana. Mwa anthu 29 omwe aphedwa pa chiwembuchi akuti ena ndi ana. Pakadali pano malipoti akusonyeza kuti zigawenga za Islamic State(IS) ndi zimene zachita chiwembuchi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>