Msodzi wina wavulala kwambiri mdziko la AUSTRALIA boti lomwe amapalasa mutalowa chi nsomba chotchedwa shark cholemera makilogram 200.
Malinga ndi malipoti a BBC mwamunayu TERRY SELWOOD(SIWUDU) wa zaka 73 zakubadwa wavulala kwambiri kaamba koti chinsombachi chitalowa mu botilo, chinamumenya kwambiri ndi chipsepse chake. Zitachitika izi a SELWOOD anakuwa kuti anthu adzawathandize ndipo pomwe anthu opulumutsa anzawo pamadzi anafika anapeza msodziyu atavulazidwa kwambiri. Pakadali pano a Selwdood akuti akupezako bwino atalandira thandizo la mankhwala pa chipatala china mdzikomo.