Amsembe m’dziko muno awapempha kuti adzizipeleka pofalitsa mauthenga a ntchito zokweza bungwe la catholic charismatic renewal ndi cholinga choti lifalikire ponseponse mdziko muno.
Bambo Bernard Tiyesi omwe anakayimilira dziko lino pa mwambo wa chikondwelero choti bungweli latha zaka 50 chilikhadzikitsileni ndi omwe anena izi pomwe amafotokozera Radio Maria Malawi zina mwa zomwe aphunzira pa ulendowu.
Mwambowu unachitika pa 4 June 2017 ku Rome m’dziko la Italy lomwenso linali tsiku la chaka cha kutsika kwa mzimu woyera kwa apostoli (pentecost sunday).Akhristu komanso ansembe amayiko osiyanasiyana ndi omwe anali nawo ku msonkhanowu.
Bambo tiyesi anati bungwe la charismatic mu mpingo wakatolika ndi la mphamvu kwambiri m’mayiko ena kamba koti amsembe ndi atumiki ena ampingo amadzipelekanso polimbikitsa ntchito za bungweli lomwe likuthandiza kuzamitsa moyo wauzimu pakati pa akhiristu ambiri mu mpigowu.